Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

June 17-23

MASALIMO 51-53

June 17-23

Nyimbo Na. 89 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Kodi Mungatani Kuti Mupewe Kuchita Machimo Akuluakulu?

(10 min.)

Musamadzidalire; munthu aliyense akhoza kulakwitsa (Sl 51:5; 2Ak 11:3)

Muzichita zimene zingakuthandizeni kukhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova (Sl 51:6; w19.01 15 ¶4-5)

Muziyesetsa kuti musamalakelake kapena kuganizira zinthu zoipa (Sl 51:10-12; w15 6/15 14 ¶5-6)

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 52:2-4​—Kodi lembali likufotokoza zotani zokhudza Doegi? (it-1 644)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(2 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. (lmd phunziro 7 mfundo 3)

5. Ulendo Woyamba

(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 4 mfundo 4)

6. Ulendo Wobwereza

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. M’phunzitseni za dzina la Mulungu. (lmd phunziro 9 mfundo 5)

7. Kuphunzitsa Anthu

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 115

8. Zomwe Mungachite Kuti Mukonze Zomwe Mwalakwitsa

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Ngakhale titayesetsa bwanji, tonsefe timalakwitsa zinthu zina. (1Yo 1:8) Ndiye zikachitika, tisamalole kuti manyazi kapena mantha atilepheretse kubwerera kwa Yehova kuti atikhululukire komanso atithandize. (1Yo 1:9) Nthawi zonse kupemphera kwa Yehova kumakhala chinthu choyamba chomwe munthu angachite kuti akonze zomwe walakwitsa.

Werengani Salimo 51:1, 2, 17. Kenako funsani funso ili:

  • Kodi mawu a Davidewa angatilimbikitse bwanji kubwerera kwa Yehova kuti atithandize pamene tachita tchimo lalikulu?

Onerani VIDIYO yakuti Moyo Wanga Wachinyamata​—Ndingatani Kuti Ndikonze Zomwe Ndinalakwitsa M’mbuyo? Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa:

  • Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinachititsa Thalila ndi José kuti alakwitse zinthu?

  • Kodi anachita zotani kuti akonze zimene analakwitsazo?

  • Kodi kuchita zimenezo kunawathandiza bwanji?

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 129 ndi Pemphero