Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

May 20-26

MASALIMO 40-41

May 20-26

Nyimbo Na. 102 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuthandiza Ena?

(10 min.)

Tikamathandiza ena timakhala osangalala (Sl 41:1; w18.08 22 ¶16-18)

Yehova amathandiza anthu amene amathandiza ena (Sl 41:2-4; w15 12/15 24 ¶7)

Tikamathandiza ena timachititsa kuti Yehova atamandike (Sl 41:13; Miy 14:31; w17.09 12 ¶17)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi pali aliyense mumpingo wathu amene ndingamuthandize kudziwa mmene angamagwiritsire ntchito JW Library?

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 40:5-10​—Kodi pemphero la Davide limatiphunzitsa chiyani zokhudza kuzindikira udindo womwe Yehova ali nawo monga Wolamulira Wamkulu? (it-2 16)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Yambani kukambirana ndi munthu amene akuoneka kuti akusangalala. (lmd phunziro 2 mfundo 3)

5. Ulendo Woyamba

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Yambani kukambirana ndi munthu amene akuoneka kuti wakhumudwa. (lmd phunziro 3 mfundo 5)

6. Kuphunzitsa Anthu

(5 min.) lff phunziro 14 mfundo 6. Kambiranani mfundo imodzi yopezeka mu nkhani yakuti “Tizitamanda Yehova Mumpingo” yomwe ili pa gawo lakuti “Onani Zinanso” ndi wophunzira amene amazengereza kuyankha pamisonkhano. (th phunziro 19)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 138

7. Tizichitira Zabwino Anthu Achikulire

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Yehova amayamikira kwambiri zonse zimene achikulire okhulupirika amachita mumpingo, choncho ifenso tiyenera kumawayamikira. (Ahe 6:10) Kwa zaka zambiri, iwo achita zambiri pophunzitsa, kuthandiza komanso kulimbikitsa Akhristu anzawo. Sitikukayikira kuti inunso mukukumbukira mmene anakuthandizirani. Kodi mungawasonyeze bwanji kuti mumawayamikira chifukwa cha zonse zomwe akhala akuchita mumpingo?

Onerani VIDIYO yakuti Tizichitira Zabwino Abale ndi Alongo Athu. Kenako funsani omvera mafunso awa:

  • Kodi Ji-Hoon anaphunzira chiyani kuchokera kwa M’bale Ho-jin Kang?

  • Kodi achikulire a mumpingo wanu mumawayamikira chifukwa cha zinthu ziti?

  • Kodi tingaphunzirepo chiyani kuchokera mu fanizo la Msamariya Wachifundo?

  • N’chifukwa chiyani mukuona kuti anali maganizo abwino kuti Ji-Hoon azikhala ndi anthu ena akamathandiza M’bale Ho-jin Kang?

Tikamaganizira kwambiri zimene anthu achikulire mumpingo wathu amafunikira, tikhoza kupeza njira zambiri za mmene tingawathandizire. Mukaona kuti enaake akufunika thandizo, muziganizira zimene mungachite kuti muwathandize.​—Yak 2:15, 16.

Werengani Agalatiya 6:10. Kenako funsani omvera funso ili:

  • Kodi ndi zinthu zabwino ziti zomwe mungachitire achikulire a mumpingo wanu?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero