Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

May 27–June 2

MASALIMO 42-44

May 27–June 2

Nyimbo Na. 86 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Tizigwiritsa Ntchito Mokwanira Malangizo Omwe Yehova Amatipatsa

(10 min.)

Tizilambira Yehova limodzi ndi anzathu, makamaka pamasom’pamaso ngati zingatheke (Sl 42:4, 5; w06 6/1 9 ¶4)

Tizipemphera tisanayambe kuphunzira Mawu a Mulungu (Sl 42:8; w12 1/15 15 ¶2)

Tizilola kuti choonadi cha m’Baibulo chizitsogolera zonse zimene timachita pa moyo wathu (Sl 43:3)

Malangizo omwe Yehova amatipatsa amatithandiza kupirira mayesero komanso kuti tisaiwale lonjezo lathu loti tidzamutumikira mpaka kalekale.​—1Pe 5:10; w16.09 5 ¶11-12.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 44:19​—Kodi mawu akuti “kumalo amene mimbulu imakhala” amanena za chiyani? (it-1 1242)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 5 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(5 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Muitanireni kuti adzamvetsere nkhani ya onse mlungu wotsatira. Gwiritsani ntchito vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? (lmd phunziro 7 mfundo 5)

6. Nkhani

(3 min.) lmd zakumapeto A mfundo 4​—Mutu: Aliyense Adzakhala Ndi Moyo Wathanzi. (th phunziro 2)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 21

7. Muzisankha Zinthu Mwanzeru pa Nkhani ya Ntchito ndi Maphunziro

(15 min.) Nkhani yokambirana

Achinyamata, kodi mukuganiza zodzachita chiyani mukadzamaliza sukulu? N’kutheka kuti mukuganizira za ntchito inayake imene ingamadzakupatseni mpata wochita upainiya. Kapena mwina mukuganizira za maphunziro enaake amene angakuthandizeni kupeza luso, satifiketi kapena kupeza dipuloma zomwe zingakuthandizeni kuti mudzapeze ntchito imene mukufunayo. Imeneyi ndi nthawi yosangalatsa kwambiri pa moyo wanu. Komabe, mukhoza kusokonezeka n’kulephera kusankha bwino zinthu, kapena kusankha zinazake pongofuna kusangalatsa anzanu. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kusankha zinthu mwanzeru?

Werengani Mateyu 6:32, 33. Kenako funsani omvera mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi zolinga zauzimu m’maganizo tisanasankhe zochita pa nkhani ya ntchito ndi maphunziro?

  • Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kugwiritsa ntchito mfundo yopezeka pa lemba la Mateyu 6:32, 33?​—Sl 78:4-7

Tizikhala osamala kuti tisalole kuti kukonda kwambiri chuma kapena kufuna kutchuka kutilepheretse kusankha bwino zinthu. (1Yo 2:15, 17) Tizikumbukira kuti kukhala ndi chuma chambiri kungalepheretse munthu kulandira uthenga wa Ufumu. (Lu 18:24-27) Kufunafuna chuma sikuyendera limodzi ndi kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kapena kusangalatsa Yehova.​—Mt 6:24; Mko 8:36.

Onerani VIDIYO yakuti Samalani Kuti Musamadalire Zinthu Zimene Zimatha​—Chuma. Kenako funsani omvera funso ili:

  •   Kodi lemba la Miyambo 23:4, 5 lingakuthandizeni bwanji kusankha zinthu mwanzeru?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 10 ¶5-12

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 47 ndi Pemphero