Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

May 6-12

MASALIMO 36-37

May 6-12

Nyimbo Na. 87 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. ‘Musamakhumudwe Chifukwa cha Anthu Oipa’

(10 min.)

Anthu oipa amachititsa kuti tizimva kupweteka komanso tizivutika (Sl 36:1-4; w17.04 10 ¶4)

Kukwiyira “anthu oipa” kungativulaze (Sl 37:1, 7, 8; w22.06 10 ¶10)

Kukhulupirira malonjezo a Yehova kumatipatsa mtendere (Sl 37:10, 11; w03 12/1 13 ¶20)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndimathera nthawi yambiri ndikuonera nkhani zachiwawa?’

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 36:6​—Kodi yemwe analemba salimoli ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti chilungamo cha Yehova chili ngati “mapiri akuluakulu [kapena kuti, “ngati mapiri a Mulungu,” mawu a m’munsi]”? (it-2 445)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 1 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pemphani munthu amene anakanapo kuphunzira Baibulo kuti muziphunzira naye. (lmd phunziro 9 mfundo 4)

6. Nkhani

(5 min.) ijwbv 45​—Mutu: Kodi lemba la Salimo 37:4 limatanthauza chiyani? (th phunziro 13)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 33

7. Kodi Mwakonzekera “Nthawi ya Mavuto”?

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Ngozi zam’chilengedwe kapena zoyambitsidwa ndi anthu zimachititsa kuti abale ndi alongo padziko lonse azikumana ndi mavuto kuphatikizapo kuferedwa. (Sl 9:9, 10) N’zomvetsa chisoni kuti tikhoza kukumana ndi mavuto nthawi ina iliyonse, choncho tiyenera kukhala okonzeka.

Kuwonjezera pa kukonzekera, a kodi n’chiyani chingatithandize kupirira pamene kwachitika ngozi inayake?

  • Muzikonzekeretsa maganizo anu: Muzikumbukira kuti ngozi zimachitika ndipo muzidziwiratu zoyenera kuchita ngati itachitikadi. Muzipewa kukonda kwambiri zinthu zomwe muli nazo. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti muchite zinthu mwanzeru n’kumaganizira za mmene mungapulumutsire moyo wanu komanso wa anthu ena m’malo moganizira kwambiri za mmene mungapulumutsire katundu wanu. (Ge 19:16; Sl 36:9) Komanso zidzakuthandizani kuti pambuyo pa ngoziyo, musamayembekezere zimene sizingachitike komanso kuti musakhale ndi nkhawa kwambiri chifukwa cha zinthu zomwe mwataya.​—Sl 37:19

  • Muzikonzekera mwauzimu: Muzikhulupirira kuti Yehova akhoza kukuthandizani ndipo ndi wofunitsitsa kuchita zimenezo. (Sl 37:18) Ngozi isanachitike, muzidzikumbutsa mobwerezabwereza kuti Yehova adzakutsogolerani komanso kukuthandizani ngakhale pamene mwataya katundu wanu yense.​—Yer 45:5; Sl 37:23, 24

Tikamaganizira za malonjezo a Yehova, iye amakhala ‘malo athu achitetezo champhamvu pa nthawi ya mavuto.’​—Sl 37:39.

Onerani VIDIYO yakuti Kodi Mwakonzeka Kukumana ndi Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi? Kenako funsani omvera mafunso awa:

  • Kodi Yehova angatithandize bwanji pa nthawi ya ngozi?

  • Kodi tingakonzekere bwanji?

  • Kodi tingathandize bwanji anthu amene akhudzidwa ndi ngozizi?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 9 ¶8-16

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 57 ndi Pemphero