Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Buku Lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa?

Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Buku Lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa?

Bukuli limaphunzitsa mfundo zofanana ndi za m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo ndondomeko yake ndi yofanananso. Komabe buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa lili ndi mawu osavuta komanso limafotokoza zinthu m’njira yosavuta kumva. Linalembedwera anthu amene angavutike kumvetsa mfundo za m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. M’malo mokhala ndi zakumapeto, buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa lili ndi mawu akumapeto omwe amafotokoza mosavuta mawu ena komanso mfundo zina zopezeka m’bukuli. Lilibenso mafunso akumayambiriro kwa mutu uliwonse komanso bokosi la mfundo zobwereza. M’malomwake, kumapeto kwa mutu uliwonse kuli mfundo zachidule za m’mutuwo. Mofanana ndi zimene tinkachita ndi buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, tikhoza kugawira buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa nthawi iliyonse ngakhale kuti si limene tikugawira m’mwezi umenewo. Koma kodi tingagwiritse ntchito bwanji zinthu za m’bukuli pophunzira Baibulo ndi munthu?

MFUNDO ZACHIDULE: Pophunzitsa anthu ambiri, tidzagwiritsa ntchito njira yowerenga kaye ndime kenako n’kufunsa funso. Koma kodi tingatani ngati munthu amene tikuphunzira naye sadziwa bwino chinenerocho kapena amavutika kuwerenga? Tikhoza kumaphunzira naye pongogwiritsa ntchito mfundo zachidule zimene zili kumapeto kwa mutu uliwonse n’kumulimbikitsa kuti awerenge payekha ndime za m’mutuwo. Nthawi zambiri mfundo iliyonse ya pa mfundo zachidule ikhoza kutenga maminitsi 15 okha basi kuti tiphunzitse munthu. Popeza kuti mfundo zachidule sizikhala ndi mfundo zonse zimene zili m’mutuwo, tiyenera kukonzekera bwino n’kumaganizira mfundo zomwe zingathandize munthuyo. Koma ngati tikuphunzitsa munthu pogwiritsa ntchito ndime zonse za m’mutuwo, tikhoza kugwiritsa ntchito mfundo zachidule pobwereza zomwe taphunzira.

MAWU AKUMAPETO: Mawu akumapeto analembedwa mogwirizana ndi ndondomeko ya mitu. Tikhoza kusankha ngati tikufuna kukambirana mawu akumapeto tikamaphunzira ndi munthu kapena ayi.