2 YOHANE 1-13; 3 YOHANE 1-14–YUDA 1-25
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |Tiyenera Kuchita Khama Kuti Tikhalebe m’Choonadi
Yesu anapereka malangizo akuti: “Yesetsani mwamphamvu kulowa pakhomo lopapatiza.” (Luka 13:24) Mawu a Yesuwa akusonyeza kuti munthu amafunika kuchita khama kuti akhale paubwenzi ndi Mulungu. Yuda, yemwe anali m’bale wake wa Yesu anauziridwa kulemba mfundo yofanana ndi imeneyi. Iye ananena kuti tiyenera “kumenya mwamphamvu nkhondo yachikhulupiriro.” Choncho m’pofunika khama kuti tizichita zotsatirazi:
-
Kupewa chiwerewere.—Yuda 6, 7
-
Kulemekeza omwe ali ndi udindo.—Yuda 8, 9
-
Kulimbitsa chikhulupiriro chathu “choyera kopambana,” pa zinthu zomwe timaphunzira.—Yuda 20, 21