Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 1-3

“Ndikudziwa Ntchito Zako”

“Ndikudziwa Ntchito Zako”

1:20; 2:1, 2

  • “Nyenyezi 7”: Odzozedwa omwe ndi akulu komanso zingatanthauze akulu ena onse

  • “M’dzanja [la Yesu] lamanja”: Yesu ali ndi udindo wotsogolera komanso kuchita chilichonse ndi nyenyezi zimenezi. Ngati mkulu wina sakuchita bwino, Yesu amadziwa njira komanso nthawi yoyenera kumuthandizira

  • “Zoikapo nyale 7 zagolide”: Mpingo wachikhristu. M’chihema, zoikapo nyale zinkathandiza kuti kuwala kwa nyale kuzionekera. Mpingo wachikhristu nawonso umathandiza kuti kuwala kwa choonadi kuzionekera. (Mat. 5:14) Ndiponso Yesu ‘amayenda’ pakati pa zoikapo nyale m’njira yakuti iye amayang’anira ntchito zomwe zimachitika m’mipingo yonse