Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Yehova Amadziwa Zimene Timafunikira

Yehova Amadziwa Zimene Timafunikira

Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatipatsa chakudya “pa nthawi yoyenera.” Zimenezi ndi umboni wakuti Yehova amene akutsogolera kapoloyu amadziwa zimene timafunikira pa moyo wathu wauzimu. (Mat. 24:45) Misonkhano yachigawo komanso misonkhano yathu yamkati mwa mlungu, ndi zina zomwe zimatitsimikizira zimenezi.

ONERANI VIDIYO YAKUTI LIPOTI LA KOMITI YOPHUNZITSA LA 2017, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ndani amene ayenera kulemekezedwa chifukwa cha misonkhano yachigawo ya pa nthawi yake yomwe timasangalala nayo, ndipo n’chifukwa chiyani?

  • Kodi ntchito yokonzekera msonkhano wachigawo imayamba liti?

  • Kodi nkhani za pamsonkhano wachigawo zimasankhidwa bwanji?

  • Kodi pamakhala ntchito yotani pokonza msonkhano wachigawo?

  • Kodi njira zophunzitsira ku sukulu ya Giliyadi zimagwiritsidwa ntchito bwanji pokonza misonkhano ya mkati mwa mlungu?

  • Kodi madipatimenti osiyanasiyana amathandizana bwanji pokonza ndandanda yautumiki?

Kodi inuyo mumachita zotani poyamikira zinthu zauzimu zomwe Yehova amatipatsa?