Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 4-6

Anthu 4 Okwera Pamahatchi

Anthu 4 Okwera Pamahatchi

6:2, 4-6, 8

Yesu ‘anapita kukagonjetsa adani ake’ pamene anamenya nkhondo yolimbana ndi Satana komanso ziwanda zake n’kuwagwetsera padziko lapansi. Iye akupitirizabe kugonjetsa adani ake pothandiza komanso kuteteza atumiki ake m’masiku otsiriza ano. Komabe adzamaliza ntchito yolimbana ndi adaniwo akadzagonjetsa okwera pamahatchi atatu enawo. Iye adzachita zimenezi pankhondo ya Aramagedo ndipo kenako adzakonza zonse zomwe okwera pamahatchi atatu aja anawononga.