MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Yehova Amakonda Munthu Wopereka Mokondwera
Lemba la 2 Akorinto 9:7, limati: “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” Masiku ano tili ndi njira zosavuta zomwe tingaperekere zopereka zathu. Mwachitsanzo, tikhoza kupereka kudzera pa intaneti pofuna kuthandiza pa ntchito zagulu lathu. Ntchitozi zingakhale zimene zikuchitika m’dziko lanu kapena padziko lonse.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MMENE MUNGAPEREKERE ZOPEREKA PA ZIPANGIZO ZA MAKONO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi tingadziwe bwanji njira zina zomwe zili m’dziko lathu zokhudza mmene tingaperekere ndalama kudzera pazipangizo zamakono?
-
Kodi anthu ena apindula bwanji chifukwa chopereka zopereka zawo kudzera pazipangizo zamakono?
-
Kodi pali njira zinanso ziti zomwe tingaperekere zopereka zathu?
-
Kodi tingatani ngati sitikudziwa mmene tingagwiritsire ntchito zipangizo zamakonozi tikafuna kupereka zopereka zathu?