November 4-10
1 YOHANE 1-5
Nyimbo Na. 122 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Musamakonde Dziko Kapena Zinthu za M’dziko”: (10 min.)
[Onerani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 1 Yohane.]
1 Yoh. 2:15, 16—“Chilichonse cha m’dziko . . . sizichokera kwa Atate, koma kudziko” (w05 1/1 10 ¶13)
1 Yoh. 2:17—Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake (w13 8/15 27 ¶18)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
1 Yoh. 2:7, 8—Kodi lamulo limene Yohane analitchula limakhala bwanji lakale komanso latsopano? (w13 9/15 10 ¶14)
1 Yoh. 5:16, 17—Kodi ndi tchimo liti limene ndi “lobweretsa imfa”? (it-1 862 ¶5)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) 1 Yoh. 1:1–2:6 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kulankhula ndi Mtima Wonse, kenako kambiranani phunziro 11 m’kabuku ka Kuphunzitsa.
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w04 10/1 29—Mutu: Kodi Yohane Ankatanthauza Chiyani pa 1 Yohane 4:18, Pamene Ananena Kuti “Chikondi Chimene Chili Chokwanira Chimathetsa Mantha”? (th Phunziro 7)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Musamatengere Maganizo a M’dzikoli Mukamakonzekera Ukwati”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Ukwati Umene Umalemekeza Yehova.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 58
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 34 ndi Pemphero