Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Musamatengere Maganizo a M’dzikoli Mukamakonzekera Ukwati

Musamatengere Maganizo a M’dzikoli Mukamakonzekera Ukwati

Akhristu amene akukonzekera kukwatirana amakhala ndi zinthu zambiri zoti asankhe. Nthawi zina angakakamizike kuti adzakhale ndi ukwati wapamwamba potengera maukwati ena a m’dera lawo. Nthawi zinanso anzawo komanso achibale awo angawakakamize kuti adzachite zinazake. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe zingawathandize kukonzekera bwino tsiku la ukwati wawo kuti asadzadziimbe mlandu kapena kunong’oneza bondo?

ONERANI VIDIYO YAKUTI UKWATI UMENE UMALEMEKEZA YEHOVA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi mfundo za m’Malembawa zinathandiza bwanji Nick ndi Juliana?

  • N’chifukwa chiyani Akhristu omwe akufuna kukwatirana ayenera kusankha m’bale wokhulupirika kuti adzakhale “woyang’anira phwando” la ukwati wawo?​—Yoh. 2:9, 10.

  • N’chifukwa chiyani Nick ndi Juliana anasankha kuchita zinthu zosiyana ndi anthu ena paukwati wawo?

  • Kodi ndi ndani ali ndi udindo wosankha mmene mwambo komanso phwando laukwati lidzakhalire?​—w06 10/15 25 ¶10.