November 2-8
EKISODO 39-40
Nyimbo Na. 89 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mose Anatsatira Malangizo Mosamala Kwambiri”: (10 min.)
Eks 39:32—Mose anatsatira mosamala kwambiri malangizo ochokera kwa Yehova okhudza kumanga chihema (w11 9/15 27 ¶13)
Eks 39:43—Chihema chitamangidwa, Mose anakachiona kuti adziwe ngati omanga anatsatira malangizo
Eks 40:1, 2, 16—Mose anaimika chihema mogwirizana ndi malangizo a Yehova (w05 7/15 27 ¶3)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Eks 39:34—Kodi n’kutheka kuti Aisiraeli anapeza bwanji chikopa cha akatumbu? (it-2 884 ¶3)
Eks 40:34—Mtambo utayamba kuphimba chihema, kodi zinkasonyeza chiyani? (w15 7/15 21 ¶1)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Eks 39:1-21 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi koma muziimitsa nthawi iliyonse pamene pali chizindikiro chosonyeza kuti muime ndipo funsani omvera mafunso omwe ali m’vidiyoyi. Kambiranani nawo zimene tingachite kuti tipewe kukhala mbali ya dziko ngati mwininyumba akufuna kukambirana nafe nkhani zandale kapena nkhani zina zimene anthu akutsutsana m’dzikoli.
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba ndipo muyankhe funso la mwininyumba lokhudza mmene mumaonera munthu wina wandale kapena nkhani ina yandale. (th phunziro 12)
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w16.04 29 ¶8-10—Mutu: Kodi Tingapewe Bwanji Kukhala Mbali ya Dziko pa Zimene Timaganiza Komanso Kulankhula? (th phunziro 14)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Tizimvetsera Mwatcheru (Mt 13:16): (15 min.) Onerani vidiyoyi. Kenako funsani mafunso awa: N’chifukwa chiyani tiyenera kumvetsera mwatcheru? Kodi lemba la Maliko 4:23, 24 limatanthauza chiyani? Kodi ndi chitsanzo chiti chimene chingatithandize kumvetsa bwino Aheberi 2:1? Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikumvetsera mwatcheru?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (Osapitirira 30 min.) jy mutu 107
Mawu Omaliza (Osapitirira 3 min.)
Nyimbo Na. 9 ndi Pemphero