CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kuleza Mtima kwa Yehova Kuli ndi Malire
Yehova analola kuti Asiriya agonjetse Aisiraeli (2Mf 17:5, 6; it-2 908 ¶5)
Yehova analanga anthu ake chifukwa ankapitiriza kuchita zinthu zoipa (2Mf 17:9-12; it-1 414-415)
Yehova anachita zinthu moleza mtima ndi Aisiraeli ndipo anawachenjeza mobwerezabwereza (2Mf 17:13, 14)
Atate wathu wachikondi Yehova, amachita zinthu moleza mtima ndi anthu opanda ungwirofe. (2Pe 3:9) Komabe, kuti akwaniritse cholinga chake, posachedwapa achitapo kanthu ndipo awononga anthu onse oipa. Kodi zimenezi zingatilimbikitse bwanji kuti tizikonza zimene timalakwitsa komanso kulalikira uthenga wabwino mwamsanga?