Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muziyembekezera Mapeto a Dzikoli Molimba Mtima

Muziyembekezera Mapeto a Dzikoli Molimba Mtima

Posachedwapa, Yehova asiya kuchita zinthu moleza mtima ndi dzikoli. Zipembedzo zoipa ziwonongedwa, mgwirizano wa mayiko uwukira anthu a Mulungu ndipo Yehova awononga anthu oipa pa nkhondo ya Aramagedo. Akhristu akuyembekezera mwachidwi nthawi yapadera komanso yosangalatsayi.

Kunena zoona sitikudziwa zonse zimene zidzachitike pa chisautso chachikulu. Mwachitsanzo, sitikudziwa nthawi yeniyeni imene chidzayambe. Sitikudziwa kuti maboma adzapereka zifukwa zotani zomwe zidzawachititse kuti aukire zipembedzo. Sitikudziwa kuti anthu a Mulungu adzaukiridwa kwa nthawi yaitali bwanji komanso kuti zidzachitika motani. Sitikudziwanso kuti Yehova adzagwiritsa ntchito njira yotani powononga anthu oipa pa Aramagedo.

Komabe, Malemba amatifotokozera zonse zomwe tikufunikira kuti tidzathe kukhala olimba mtima pa nthawiyi. Mwachitsanzo, timadziwa kuti tikukhala kumapeto kwa “masiku otsiriza.” (2Ti 3:1) Tikudziwa kuti masiku amene chipembedzo chonyenga chidzakhale chikuwonongedwa “adzafupikitsidwa” n’cholinga choti chipembedzo choona chisawonongedwe nawo. (Mt 24:22) Tikudziwa kuti Yehova adzapulumutsa anthu ake. (2Pe 2:9) Tikudziwanso kuti amene Yehova anasankha kuti adzawononge anthu oipa n’kupulumutsa akhamu lalikulu pa Aramagedo ndi wolungama komanso wamphamvu kwambiri.​—Chv 19:11, 15, 16.

Sitikukayikira kuti pazochitika zimenezi, ena “adzakomoka chifukwa cha mantha.” Komabe tikamawerenga n’kumaganizira mozama mmene Yehova wakhala akupulumutsira anthu ake m’mbuyomu, komanso zimene watiuza kuti zichitika m’tsogolomu, tikhoza ‘kudzaimirira chilili ndi kutukula mitu yathu’ molimba mtima podziwa kuti chipulumutso chathu chayandikira.​—Lu 21:26, 28.