MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zimene Zingatithandize Kuti Tisamazengereze Pochita Zinthu
Munthu wozengereza amasunthira patsogolo zinthu zimene amafunika kuchita panthawiyo. Zimenezi si zomwe Yehu anachita atapatsidwa utumiki ndi Yehova kuti akaphe anthu onse a m’nyumba ya Ahabu. (2Mf 9:6, 7, 16) Anthu ena amanena kuti: “Mwina ndibatizidwa zaka zikubwerazi.” “Ndiyamba kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku posachedwapa.” “Ndidzayamba upainiya n’kadzapeza ntchito yabwino.” Malemba angatithandize kupewa kuzengereza tikamachita zinthu zokhudza kulambira.
Kodi malemba otsatirawa angatithandize bwanji kupewa kuchita zinthu mozengereza?