CHUMA CHOPEZEKA MMAWU A MULUNGU
“Nyumba Yonse ya Ahabu Ifafanizidwe”—2Mf 9:8
UFUMU WA YUDA
Yehosafati anakhala mfumu
c. 911 B.C.E: Yehoramu (mwana wa Yehosafati; mwamuna wa Ataliya, mwana wamkazi wa Ahabu ndi Yezebeli) anayamba kulamulira yekha
c. 906 B.C.E: Ahaziya (mdzukulu wa Ahabu ndi Yezebeli) anakhala mfumu
c. 905 B.C.E: Ataliya anapha ana onse a m’banja la chifumu ndipo anayamba kulamulira. Mdzukulu wake mmodzi yekha Yehoasi ndi amene anapulumuka ndipo anabisidwabe kwa kanthawi ndi Mkulu wa Ansembe Yehoyada.—2Mf 11:1-3
898 B.C.E: Yehoasi anakhala mfumu. Mfumukazi Ataliya inaphedwa ndi Mkulu wa Ansembe Yehoyada.—2Mf 11:4-16
UFUMU WA ISIRAELI
c. 920 B.C.E: Ahaziya (mwana wa Ahabu ndi Yezebeli) anakhala mfumu
c. 917 B.C.E: Yehoramu (mwana wa Ahabu ndi Yezebeli) anakhala mfumu
c. 905 B.C.E: Yehu anapha Mfumu Yehoramu ya Isiraeli ndi azichimwene ake, mayi ake a Yehoramu (Yezebeli) komanso Mfumu Ahaziya ya ku Yuda ndi azichimwene ake.—2Mf 9:14–10:17
c. 904 B.C.E: Yehu anayamba kulamulira monga mfumu