MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Khalani Opatsa”
Yesu ananena kuti munthu wopatsa amachititsanso ena kukhala opatsa. (Lu 6:38) Mukakhala ndi chizolowezi chopatsa ena zinthu, mumalimbikitsa abale ndi alongo anu kukhala okoma mtima komanso opatsa.
Yehova amayembekezera kuti anthu amene amamulambira azipereka mokondwera. Iye amaona anthu amene ali ndi mtima wopatsa komanso omwe amathandiza Akhristu anzawo amene akuvutika ndipo adzawapatsa mphoto.—Miy 19:17.
ONERANI VIDIYO YAKUTI TIKUKUTHOKOZANI CHIFUKWA CHA MTIMA WANU WOPATSA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi zopereka zanu zimagwiritsidwa ntchito bwanji pothandiza abale ndi alongo anu?
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kukhala ndi mtima wopatsa posatengera kukula kwa mphatso zathu?—Onaninso nkhani ya pa jw.org yakuti “Zimene Ena Ali Nazo Zimathandizira pa Zimene Ena Akusowa.”