Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

December 23-29

SALIMO 119:121-176

December 23-29

Nyimbo Na. 31 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Kodi Tingatani Kuti Tizipewa Mavuto?

(10 min.)

Tizikonda malamulo a Mulungu (Sl 119:127; w18.06 17 ¶5-6)

Tizidana ndi zoipa (Sl 119:128; w93 4/15 17 ¶12)

Tizimvera Yehova ndipo tizipewa kulakwitsa zinthu ngati mmene amachitira ‘anthu osadziwa zambiri’ (Sl 119:130, 133; Miy 22:3)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndi zinthu ziti zimene ndiyenera kusintha kuti ndizikonda kwambiri malamulo a Mulungu kapena ndizidana kwambiri ndi zoipa?’

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 119:160—Mogwirizana ndi vesili, kodi tiyenera kukhala otsimikiza za chiyani? (w23.01 2 ¶2)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 1 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Musonyezeni mmene angapezere nkhani imene ingamusangalatse pa jw.org. (lmd phunziro 8 mfundo 3)

6. Kuphunzitsa Anthu

(5 min.) Kambiranani ndi wophunzira Baibulo amene safika pamisonkhano mokhazikika. (lmd phunziro 12 mfundo 4)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 121

7. Musalole Kuti Ndalama Zikubweretsereni Mavuto Opeweka

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Anthu amene amachita zinthu chifukwa chokonda ndalama ‘amadzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.’ (1Ti 6:9, 10) M’munsimu muli mavuto ena omwe tikhoza kuwapewa, koma tingakumane nawo ngati timakonda kwambiri ndalama n’kulola kuti zizitilamulira.

  • Sitingathe kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.—Mt 6:24

  • Sitingakhale okhutira.—Mla 5:10

  • Zikhoza kukhala zovuta kwambiri kuti tipewe kuchita zoipa monga kunama, kuba ngakhalenso chinyengo. (Miy 28:20) Kugonja pa mayesero oterewa kungachititse kuti tizidziimba mlandu, tikhale ndi mbiri yoipa komanso Yehova asiye kutikonda

Werengani Aheberi 13:5, kenako kambiranani funso ili:

  • Kodi ndalama tiziziona motani kuti tipewe mavuto, nanga n’chifukwa chiyani?

Ngakhale titakhala kuti sitikonda ndalama, tikhoza kukumanabe ndi mavuto ngati sitimazigwiritsa ntchito mwanzeru.

Onerani VIDIYO YAMAKATUNI yakuti Mungatani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama Zanu? Kenako funsani mafunso otsatirawa:

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kupanga bajeti, nanga tingaipange bwanji?

  • N’chifukwa chiyani ndi bwino kumasunga ndalama zina?

  • N’chifukwa chiyani ndi nzeru kumapewa ngongole zosafunika?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero