December 30, 2024–January 5, 2025
MASALIMO 120-126
Nyimbo Na. 144 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Anafesa Mbewu Akukhetsa Misozi, N’kukolola Akusangalala
(10 min.)
Aisiraeli anasangalala kwambiri pamene anamasulidwa ku ukapolo ku Babulo kuti akabwezeretse kulambira koona (Sl 126:1-3)
Amene anabwerera ku Yudeya n’kutheka kuti analira chifukwa cha ntchito yowawa imene ankafunika kugwira (Sl 126:5; w04 6/1 16 ¶10)
Koma anthuwo sanasiye ndipo analandira madalitso (Sl 126:6; w21.11 24 ¶17; w01 7/15 18-19 ¶13-14; onani chithunzi)
FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Pambuyo poti tapulumutsidwa ku dziko loipali pa Aramagedo, kodi ndi zovuta ziti zomwe tingadzakumane nazo pogwira ntchito yaikulu yokonzanso dzikoli? Nanga tidzalandira madalitso otani?
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Sl 124:2-5—Kodi tingayembekezere kuti Yehova azititeteza ngati mmene ankachitira ndi mtundu wa Aisiraeli? (cl 73 ¶15)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 124:1–126:6 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. (lmd phunziro 3 mfundo 5)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pa ulendo wapita, munthuyo anasonyeza kuti sakhulupirira Baibulo. (lmd phunziro 9 mfundo 5)
6. Kuphunzitsa Anthu
Nyimbo Na. 155
7. Tizisangalala ndi Malonjezo a Mulungu
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Yehova anakwaniritsa zimene analonjeza anthu ake omwe anali ku ukapolo ku Babulo. Iye anawalanditsa komanso kuwachiritsa mwauzimu. (Yes 33:24) N’zoonekeratu kuti anawateteza limodzi ndi ziweto zawo kuti asagwidwe ndi mikango komanso zilombo zina zolusa zomwe zinachuluka m’dziko lawo pa nthawi imene simunkakhala anthu. (Yes 65:25) Iwo ankasangalala kukhala m’nyumba zawozawo komanso kudya zipatso za m’minda yawo ya mpesa. (Yes 65:21) Mulungu anadalitsa ntchito yawo ndipo anakhala ndi moyo wautali.—Yes 65:22, 23.
Onerani VIDIYO yakuti Tizisangalala ndi Malonjezo a Mulungu Okhudza Mtendere—Kachigawo Kake. Kenako funsani mafunso otsatirawa:
-
Kodi maulosiwa akukwaniritsidwa bwanji masiku athu ano?
-
Kodi adzakwaniritsidwanso bwanji m’dziko latsopano?
-
Kodi ndi malonjezo ati amene mukuyembekezera kwambiri?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 20 ¶8-12, bokosi patsamba 161