November 18-24
MASALIMO 107-108
Nyimbo Na. 7 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. “Yamikani Yehova, Chifukwa Iye ndi Wabwino”
(10 min.)
Mofanana ndi mmene Yehova anapulumutsira Aisiraeli ku Babulo, iye anatipulumutsanso m’dziko la Satanali (Sl 107:1, 2; Akl 1:13, 14)
Chifukwa choti timayamika Yehova, timamutamanda mumpingo (Sl 107:31, 32; w07 4/15 20 ¶2)
Timayamikira kwambiri Yehova tikamaganizira zonse zimene wakhala akutichitira (Sl 107:43; w15 1/15 9 ¶4)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Sl 108:9—Kodi n’kutheka kuti palembali ankatanthauza chiyani pamene amayerekezera Mowabu ndi “beseni losambiramo” la Yehova? (it-2 420 ¶4)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 107:1-28 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. (lmd phunziro 1 mfundo 4)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Muuzeni kuti timaphunzira Baibulo ndi anthu ndipo m’patseni khadi lodziwitsa anthu za phunziro la Baibulo. (lmd phunziro 9 mfundo 3)
6. Nkhani
(5 min.) ijwyp 90—Mutu: Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangoganizira Zinthu Zolakwika? (th phunziro 14)
Nyimbo Na. 46
7. Timaimba Nyimbo Kuti Tithokoze Yehova
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Yehova atapulumutsa Aisiraeli omwe ankachita mantha m’manja mwa asilikali amphamvu a ku Iguputo pa Nyanja Yofiira, iwo anaimba nyimbo posonyeza kuthokoza. (Eks 15:1-19) Amuna ndi amene ankatsogolera poimba nyimbo yatsopanoyi. (Eks 15:21) Yesu komanso Akhristu oyambirira, nawonso ankaimba nyimbo potamanda Yehova. (Mt 26:30; Akl 3:16) Nafenso timasonyeza kuti timayamikira Yehova poimba nyimbo pamisonkhano yampingo, yadera komanso yachigawo. Mwachitsanzo, nyimbo yomwe tangoimbayi yamutu wakuti “Timakuyamikirani Yehova,” yakhala ikuimbidwa pamisonkhano yathu kuyambira mu 1966.
M’zikhalidwe zina, amuna amachita manyazi kuimba nyimbo pagulu. Anthu ena amalephera kuimba chifukwa amaona kuti mawu awo samveka bwino akamaimba. Komabe, tizikumbukira kuti kuimba pa misonkhano ndi mbali ya kulambira kwathu. Gulu la Yehova limachita khama kwambiri pokonza nyimbo zabwino komanso posankha nyimbo zoyenera zoti tiziimba pamsonkhano uliwonse. Mbali yathu ndi yosavuta. Timangofunika kuimba limodzi mogwirizana posonyeza kuti timakonda komanso timathokoza Atate wathu wakumwamba Yehova.
Onerani VIDIYO yakuti Mbiri ya Gulu Lathu—Mphatso ya Nyimbo, Mbali Yachiwiri. Kenako funsani mafunso otsatirawa:
-
Kodi ndi chinthu chosaiwalika chiti chimene chinachitika mu 1944?
-
Kodi abale athu a ku Siberia anasonyeza bwanji kuti amakonda kuimba nyimbo za Ufumu?
-
N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amaona kuti kuimba nyimbo n’kofunika kwambiri?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 18 ¶6-15