Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

November 4-10

SALIMO 105

November 4-10

Nyimbo Na. 3 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Amakumbukira Pangano Lake Mpaka Kalekale”

(10 min.)

Yehova anachita pangano ndi Abulahamu ndipo analibwerezanso kwa Isaki ndi Yakobo (Ge 15:18; 26:3; 28:13; Sl 105:8-11)

Lonjezo limeneli linkaoneka ngati silingakwaniritsidwe (Sl 105:12, 13; w23.04 28 ¶11-12)

Yehova sanaiwale pangano limene anachita ndi Abulahamu (Sl 105:42-44; it-2 1201 ¶2)


DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi kudziwa kuti Yehova ndi wodalirika kumandithandiza bwanji kuti ndizikhulupirira malonjezo a zimene zichitike m’tsogolo?’

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 105:17-19—Kodi ‘mawu a Yehova anayenga’ bwanji Yosefe? (w86 11/1 18 ¶15)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(1 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mwininyumba ndi wotanganidwa. (lmd phunziro 2 mfundo 5)

5. Ulendo Woyamba

(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mwaulemu, siyani kukambirana ndi munthu amene akufuna kukangana nanu. (lmd phunziro 4 mfundo 5)

6. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’patseni magazini imene ili ndi nkhani imene anachita nayo chidwi pa ulendo wapita. (lmd phunziro 8 mfundo 3)

7. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Muuzeni zokhudza JW Library® ndipo muthandizeni kupanga dawunilodi. (lmd phunziro 9 mfundo 5)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 84

8. Mumasonyeza Chikondi Chanu

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Tikamagwiritsa ntchito nthawi yathu, mphamvu zathu komanso ndalama zathu pa zinthu za Ufumu, timakhala tikusonyeza kuti timakonda Mwana wa Yehova, Khristu Yesu, amene anamuika pampando wachifumu. Zimenezi zimachititsa kuti tizikonda kwambiri Yehova komanso zimathandiza abale ndi alongo athu. (Yoh 14:23) Nkhani za pa jw.org zamutu wakuti “Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?,” zimasonyeza mmene zopereka zathu zimathandizira abale ndi alongo padziko lonse.

Onerani VIDIYO yakuti Zopereka Zanu Zili ndi Mphamvu. Kenako funsani mafunso otsatirawa:

  • Kodi zopereka zathu zathandiza bwanji kuti abale athu ateteze ufulu wawo wolambira?

  • Kodi kuyesetsa kuti pakhale “kufanana” pa nkhani ya ndalama, kwathandiza bwanji pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu?—2Ak 8:14

  • Kodi kugwiritsa ntchito zopereka zathu pa ntchito yomasulira Baibulo mu zilankhulo zina kwathandiza bwanji?

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 17 ¶13-19

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 97 ndi Pemphero