October 10-16
MIYAMBO 7-11
Nyimbo Na. 32 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mtima Wako Usapatuke”: (10 min.)
Miy. 7:6-12—Nthawi zambiri anthu opanda nzeru amachita zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wawo ndi Yehova (w00 11/15 29-30)
Miy. 7:13-23—Munthu akasankha zinthu mopanda nzeru akhoza kukumana ndi mavuto aakulu (w00 11/15 30-31)
Miy. 7:4, 5, 24-27—Tikakhala anzeru komanso omvetsa zinthu tidzapewa mavuto ambiri (w00 11/15 29, 31)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Miy. 9:7-9—Kodi zimene timachita tikapatsidwa malangizo zimasonyeza kuti ndife anthu otani? (w01 5/15 29-30)
Miy. 10:22—Kodi ndi madalitso ati amene Yehova akutipatsa masiku ano? (w06 5/15 26-30 ndime 3-16)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Miy. 8:22-36; 9:1-6
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Nkhani yokhudza mutu wapachikuto wa g16.5—Muitanireni munthuyo kumisonkhano yathu.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Nkhani yokhudza mutu wapachikuto wa g16.5—Muitanireni munthuyo kumisonkhano yathu.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) bhs 186-187 ndime 5-6—Muitanireni munthuyo kumisonkhano yathu.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Nyimbo Na. 83
Zimene Achinyamata Anzanu Amanena—Foni Zam’manja (Miy. 10:19): (15 min.) Nkhani yokambirana. Poyamba, onetsani vidiyo yakuti, Zimene Achinyamata Anzanu Amanena—Foni Zam’manja. Kenako kambiranani nkhani ya pa jw.org/ny yakuti, “Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Mameseji a Pafoni?” Fotokozani bwino mfundo zomwe zili pakamutu kakuti, “Zofunika Kukumbukira pa Nkhani ya Mameseji.”
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 8 ndime 17-27 komanso Mfundo Zofunika Kuziganizira patsamba 75.
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 152 ndi Pemphero
Kumbukirani: Muyenera kuika nyimboyi kuti onse amvetsere, kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo.