October 3-9
MIYAMBO 1-6
Nyimbo Na. 37 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Khulupirira Yehova ndi Mtima Wako Wonse”: (10 min.)
[Onetsani vidiyo yakuti, Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Miyambo.]
Miy. 3:1-4—Muzisonyeza kukoma mtima kosatha ndiponso choonadi (w00 1/15 23-24)
Miy. 3:5-8—Muzikhulupirira Yehova ndi mtima wonse (w00 1/15 24)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Miy. 1:7—Kodi kuopa Yehova ndi “chiyambi cha kudziwa zinthu” m’njira yotani? (w06 9/15 17 ndime 1; it-2-E 180)
Miy. 6:1-5—Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife anzeru ngati tazindikira kuti tinavomera kuchita zinthu zinazake zabizinezi tisanaziganizire bwinobwino? (w00 9/15 25-26)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Miy. 6:20-35
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Nkhani yokambirana. Pambuyo poonetsa vidiyo iliyonse ya chitsanzo cha ulaliki, kambiranani mfundo zimene tikuphunzirapo. Limbikitsani ofalitsa kuti azigwira nawo ntchito yapadziko lonse yoitanira anthu kumisonkhano yathu.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Nyimbo Na. 107
Zofunika Pampingo: (8 min.) Mukhozanso kukambirana zimene tikuphunzira mu Buku Lapachaka. (yb16 25-27)
Muzichitira Zabwino Anthu Omwe Amabwera Kumisonkhano Yathu (Miy. 3:27): (7 min.) Nkhani yokambirana. Poyamba, onetsani vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? Kenako funsani abale ndi alongo kuti afotokoze zimene tingachite kuti tizisonyeza chikondi nthawi zonse pa Nyumba ya Ufumu.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 8 ndime 1-16
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 143 ndi Pemphero