October 31–November 6
MIYAMBO 22-26
Nyimbo Na. 88 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Phunzitsa Mwana M’njira Yomuyenerera” (10 min.)
Miy. 22:6; 23:24, 25—Makolo akamaphunzitsa ana pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo, nthawi zambiri anawo akakula amakhala osangalala ndiponso odalirika (w08 4/1 16; w07 6/1 31)
Miy. 22:15; 23:13, 14—M’lembali, “ndodo” imaimira kuphunzitsa, kulangiza komanso kupereka chilango (w15 11/15 5 ndime 6; w07 2/15 27 ndime 18; w97 10/15 32; it-2-E 818 ndime 4)
Miy. 23:22—Ngakhale Ana atakula, akhoza kupindula ndi nzeru za makolo awo (w04 6/15 14 ndime 1-3; w00 6/15 21 ndime 13)
Kufufuza Mfundo Zothandiza (8 min.)
Miy. 24:16—Kodi lembali limatilimbikitsa bwanji kuti tizipirira pa mpikisano wokalandira moyo wosatha? (w13 3/15 4-5 ndime 5-8)
Miy. 24:27—Kodi lembali lili ndi mfundo yotani? (w09 10/15 12 ndime 1)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Miy. 22:1-21
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Khadi lodziwitsa anthu za JW.ORG—Kulalikira mwamwayi.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Khadi lodziwitsa anthu za JW.ORG—Muuzeni nkhani imene mudzakambirane mukadzabweranso. Pomaliza, muuzeni kuti mukufuna kumuonetsa vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) lv 179-181 ndime 18-19
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Nyimbo Na. 101
“Kodi Mukugwiritsa Ntchito Bwino Makadi Odziwitsa Anthu za JW.ORG?”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Poyamba, onetsani vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki, kenako kambiranani mfundo zimene tikuphunzirapo. Limbikitsani ofalitsa kuti azinyamula makadiwa nthawi zonse.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 10 ndime 1-11, bokosi patsamba 86.
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 146 ndi Pemphero
Kumbukirani: Muyenera kuika nyimboyi kuti onse amvetsere, kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo.