MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Akhristu Oona Amadziwika Chifukwa cha Chikondi—Musamakhale ndi Mtima Wofuna Kuchita Zofuna Zanu Zokha Komanso Musamakwiye
KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Yesu anaphunzitsa kuti ophunzira ake adzadziwika chifukwa cha chikondi. (Yoh. 13:34, 35) Kuti tisonyeze chikondi ngati mmene Yesu ankachitira, tiziganizira zofuna za ena ndipo tizipewa kukwiya.—1 Akor. 13:5.
KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?
-
Wina akanena kapena kuchita zinthu zomwe zakukhumudwitsani, muziima kaye n’kuganizira chimene chachititsa komanso zimene zingachitike ngati mutapanda kuugwira mtima.—Miy. 19:11.
-
Tizikumbukira kuti tonse ndife ochimwa, ndipo nthawi zina timachita kapena kulankhula zinthu zimene pambuyo pake timanong’oneza nazo bondo
-
Tizithetsa kusamvana mwamsanga
ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIKONDANA’—MUSAMAKHALE NDI MTIMA WOFUNA KUCHITA ZOFUNA ZANU ZOKHA KOMANSO MUSAMAKWIYE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi a Larry anatani a Tom atawauza kuti atsalire pambuyo pa misonkhano?
-
Kodi kudikira kaye asanayankhe kunawathandiza bwanji a Tom kuti augwire mtima?
-
Kodi zimene a Tom anachita poyankha mofatsa zinathandiza bwanji kuti zinthu zisafike poipa kwambiri?