October 22-28
YOHANE 15-17
Nyimbo Na. 129 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Simuli Mbali ya Dzikoli”: (10 min.)
Yoh. 15:19—Otsatira a Yesu ‘sali mbali ya dzikoli’ (“dziko” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 15:19, nwtsty)
Yoh. 15:21—Anthu amadana ndi otsatira a Yesu chifukwa cha dzina lake (“chifukwa cha dzina langa” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 15:21, nwtsty)
Yoh. 16:33—Otsatira a Yesu angathe kugonjetsa dziko ngati atamayesetsa kumutsanzira (it-1 516)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Yoh. 17:21-23—Kodi otsatira a Yesu amakhala “amodzi” m’njira yotani? (“amodzi” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 17:21, nwtsty; “akhale mu umodzi weniweni” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 17:23, nwtsty)
Yoh. 17:24—Kodi mawu akuti “musanayale maziko a dziko” akutanthauza chiyani? (“musanayale maziko a dziko” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 17:24, nwtsty)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yoh. 17:1-14
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza wachiwiri.
Ulendo Wobwereza Wachitatu: (Osapitirira 3 min.) Sankhani lemba lililonse ndipo gawirani buku kapena kabuku kamene timagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) fg phunziro 14 ¶3-4
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Akhristu Oona Amadziwika Chifukwa cha Chikondi—Muziteteza Mgwirizano Wathu Wamtengo Wapatali”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onetsani vidiyo yakuti ‘Muzikondana’—Musamasunge Zifukwa. Ngati nthawi ilipo, kambiranani mfundo za m’kabokosi kakuti “Chitsanzo cha M’Baibulo Chofunika Kuchiganizira.”
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 10, ndi bokosi lakuti “Ulendo Wosangalatsa”
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 133 ndi Pemphero