Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Akhristu Oona Amadziwika Chifukwa cha Chikondi​​—Muziteteza Mgwirizano Wathu Wamtengo Wapatali

Akhristu Oona Amadziwika Chifukwa cha Chikondi​​—Muziteteza Mgwirizano Wathu Wamtengo Wapatali

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anapempherera ophunzira ake kuti “akhale mu umodzi weniweni.” (Yoh. 17:23) Kuti tikhale ogwirizana, tiyenera kusonyezana chikondi chimene “sichisunga zifukwa.”​—1 Akor. 13:5.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Tizitsanzira Yehova poyesetsa kuona zabwino zimene anthu ena amachita

  • Tizikhululuka ndi mtima wonse

  • Tikakhululukira munthu wina, tisamalankhulenso za nkhaniyo.​—Miy. 17:9

ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIKONDANA’​—MUSAMASUNGE ZIFUKWA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • M’mbali yoyamba ya vidiyoyi, kodi Helen anasonyeza bwanji kuti ‘amasunga zifukwa’?

  • M’mbali yachiwiri ya vidiyoyi, kodi Helen anatani kuti ayambe kuona zinthu moyenera?

  • Kodi zimene anachitazi zinathandiza bwanji kuti mpingo ukhale wogwirizana?

Kodi ndi ndani amene amapwetekeka tikamasungira ena zifukwa?