Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Akhristu Oona Amadziwika Chifukwa cha Chikondi​—Muzisangalala ndi Choonadi

Akhristu Oona Amadziwika Chifukwa cha Chikondi​—Muzisangalala ndi Choonadi

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Potengera chitsanzo cha Yesu, tiyenera kumayesetsa kuchitira umboni choonadi chokhudza zolinga za Mulungu. (Yoh. 18:37) Tiyeneranso kumasangalala ndi choonadi, kulankhula zoona komanso kupitirizabe kuganizira zinthu zilizonse zoona ngakhale kuti tikukhala m’dziko limene anthu ambiri ndi achinyengo komanso opanda chilungamo.​—1 Akor. 13:6; Afil. 4:8.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Tisamamvetsere kapena kufalitsa nkhani zamiseche.​—1 Ates. 4:11

  • Tisamasangalale anthu ena akakumana ndi mavuto

  • Tizisangalala ndi zinthu zabwino komanso zolimbikitsa

ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIKONDANA’​—MUZISANGALALA NDI CHOONADI, OSATI NDI ZOSALUNGAMA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Debbie anasonyeza bwanji kuti ‘ankasangalala ndi zosalungama’?

  • Kodi Alice anasintha bwanji nkhani imene Debbie ankakamba n’kuyamba kukambirana zolimbikitsa?

  • Kodi ndi zinthu zina ziti zolimbikitsa zimene tingakambirane?

Muzisangalala ndi choonadi, osati ndi zosalungama