MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Achinyamata, Kodi Yehova Ndi Mnzanu Wapamtima?
Kodi mumafuna kuti mnzanu akhale ndi makhalidwe otani? Mwina mumafuna kuti akhale wokhulupirika, wokoma mtima komanso wopatsa. Yehova ali ndi makhalidwe onsewa. (Eks 34:6; Mac 14:17) Iye amamvetsera mukamapemphera, amakuthandizani mukamavutika komanso amakukhululukirani mukalakwitsa. (Sl 18:19, 35; 1Yo 1:9) Apa zikuonekeratu kuti Yehova ndi Mnzanu wabwino kwambiri.
Koma kodi mungatani kuti mukhale mnzake wa Yehova? Muyenera kuphunzira za iye powerenga Mawu ake. Muyeneranso kumuuza zakukhosi kwanu. (Sl 62:8; 142:2) Muzisonyeza kuti mumakonda zinthu zimene iye amaona kuti n’zofunika monga Mwana wake, Ufumu wake komanso malonjezo ake okhudza m’tsogolo. Muziuzanso anthu ena za iye. (De 32:3) Mukamayesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, iye adzakhala Mnzanu mpaka kalekale.—Sl 73:25, 26, 28.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ACHINYAMATA—“TALAWANI NDIPO MUONA KUTI YEHOVA NDI WABWINO,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi mungakonzekere bwanji kuti mudzadzipereke kwa Yehova komanso kubatizidwa?
-
Kodi anthu ena mumpingo angakuthandizeni bwanji kuti muzitumikira Yehova?
-
Kodi kulalikira kumalimbitsa bwanji ubwenzi wanu ndi Yehova?
-
Kodi pali zinthu ziti zimene mungachite potumikira Yehova?
-
Kodi mumakonda zinthu ziti zokhudza Yehova?