MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muziona Kuti Ubwenzi Wanu Ndi Yehova Ndi Wamtengo Wapatali
Atumiki a Yehovafe tili ndi mwayi wapadera. Popeza tinadzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa, timapitiriza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye, yemwe ndi Ambuye Wamkulu Koposa. Mulungu anatikokera kwa iye kudzera mwa Mwana wake. (Yoh 6:44) Komanso amamvetsera mapemphero athu.—Sl 34:15.
Kodi tingateteze bwanji ubwenzi wathu ndi Mulungu? Njira imodzi ndi kupewa kuchita zinthu zoipa zimene Aisiraeli ankachita. Atangochita pangano ndi Yehova, anapanga mwana wa ng’ombe wagolide n’kuyamba kumulambira. (Eks 32:7, 8; 1Ak 10:7, 11, 14) Tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndimachita chiyani ndikamayesedwa kuti ndichite zoipa? Kodi zochita zanga zimasonyeza kuti ndimaona kuti ubwenzi wanga ndi Yehova ndi wamtengo wapatali?’ Kukonda Atate wathu wakumwamba kudzatithandiza kuti tizipewa zinthu zimene amadana nazo.—Sl 97:10.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZITETEZA UBWENZI WANU NDI YEHOVA (AKL 3:5), KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi kusirira kwa nsanje n’kutani?
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kusirira kwa nsanje komanso kulambira mafano?
-
Kodi chigololo ndi kulambira mafano zimagwirizana bwanji?
-
N’chifukwa chiyani abale amene ali ndi udindo mumpingo ayenera kuyesetsa kupeza nthawi yocheza ndi akazi awo?