Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Zinthu Zimene Tiyenera Kupewa Tikamachititsa Phunziro la Baibulo

Zinthu Zimene Tiyenera Kupewa Tikamachititsa Phunziro la Baibulo

Tisamalankhule Kwambiri: Tikamachititsa phunziro la Baibulo, sitiyenera kufotokoza zinthu zambirimbiri. Yesu ankagwiritsa ntchito mafunso pofuna kuthandiza anthu kuganiza, n’cholinga choti adziwe zoyenera kuchita. (Mat. 17:24-27) Mafunso amathandiza kuti phunziro likhale losangalatsa. Amathandizanso kuti mudziwe ngati wophunzira wanu wamvetsa mfundo inayake komanso ngati akukhulupirira zimene waphunzirazo. (be 253 ndime 3-4) Mukafunsa funso, muzidikira kaye mpaka munthuyo atayankha. Ngati wophunzira wanuyo wayankha molakwika, sibwino kumuuza yankho lolondola. Mungamuthandize kupeza yankho lolondola pomufunsa mafunso owonjezera. (be 238 ndime 1-2) Musamalankhule mofulumira kwambiri n’cholinga choti wophunzira wanu asavutike kumvetsa mfundo zofunika.—be 230 ndime 4.

Tisamafotokoze Zinthu Zambiri Nthawi Imodzi: Tikamachititsa phunziro, tiyenera kupewa kufotokoza zonse zimene tikudziwa pa nkhaniyo. (Yoh. 16:12) M’malo mochulutsa gaga m’diwa, tingachite bwino kuthandiza wophunzira wathu kumvetsa mfundo yaikulu ya ndime imene tikukambirana. (be 226 ndime 4-5) Nthawi zina, mfundo zowonjezera, ngakhale zitakhala zosangalatsa, zimangophimba mfundo zofunika. (be 235 ndime 3) Ngati wophunzirayo wamvetsa mfundo yaikulu, tingachite bwino kupita pa ndime ina.

Tisamangophunzitsa Kuti Tithane Nazo: Cholinga chathu tikamaphunzira ndi anthu chimakhala kuwafika pamtima, osati kuphunzira ndime zambiri. (Luka 24:32) Choncho tikamaphunzira, tingachite bwino kumawerenga Malemba omwe akugwirizana kwambiri ndi nkhaniyo. (2 Akor. 10:4; Aheb. 4:12; be 144 ndime 1-3) Tingachitenso bwino kumagwiritsa ntchito zitsanzo komanso mafanizo osavuta. (be  245 ndime 2-4) Tikamakonzekera, tingachite bwino kuganizira mavuto amene wophunzira wathu akukumana nawo komanso zimene amakhulupirira. Kenako tingasankhe mfundo zomwe zingamuthandize kwambiri. Mukamaphunzira naye, mungamufunse mafunso ngati awa: “Kodi mukukhulupirira kuti zimenezi n’zoona?” “Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani za Yehova?” “Kodi mfundo imeneyi ingakuthandizeni bwanji pamoyo wanu?”—be 238 ndime 3-5; 259 ndime 1.