Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Ngati Tapeza Mwana Pakhomo Lomwe Tikufuna Kulalikira

Ngati Tapeza Mwana Pakhomo Lomwe Tikufuna Kulalikira

Tikapeza mwana pakhomo lomwe tikufuna kulalikira, tingachite bwino kumuuza kuti akaitane makolo ake. Zimenezi zingasonyeze kuti timalemekeza udindo wa makolowo. (Miy. 6:20) Ngati mwanayo watiuza kuti tilowe m’nyumba, tiyenera kukana. Ndipo akatiuza kuti makolo ake achokapo, tingachite bwino kudzapitanso ulendo wina.

Tikapeza mwana wamkulu, mwina wa zaka 15 mpaka 19, tingachitenso bwino kupempha chilolezo kwa makolo ake. Ngati makolowo palibe, tingafunse mwanayo ngati makolo ake amamulola kusankha yekha zinthu zoti aziwerenga. Akatiuza kuti amamuloleza, tingamupatse magazini kapena chinthu china choti awerenge. Tikhozanso kumuuza kuti angapeze zinthu zambiri zoti aziwerenga pa webusaiti yathu ya jw.org.

Tikamapitanso kukacheza ndi mwana amene anasonyeza chidwi, tingachite bwino kumupempha kuti tikumane ndi makolo ake. Kuchita zimenezi, kungatipatse mwayi wofotokozera makolowo chifukwa chimene tabwerera kunyumba kwawo. Tingawauzenso kuti malangizo a m’Baibulo angathandize banja lawo kuti liziyenda bwino. (Sal. 119:86, 138) Tikamachita zinthu mwaulemu kwa makolo a ana amene tawapeza tikamalalikira, zingapangitse kuti makolowo akhale ndi chidwi chofuna kumvetsera uthenga wathu. Zimenezi zingatipatse mpata wolalikira uthenga wabwino kwa banja lonse.—1 Pet. 2:12.