September 17-23
YOHANE 5-6
Nyimbo Na. 2 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Muzitsatira Yesu Muli ndi Zolinga Zabwino”: (10 min.)
Yoh. 6:9-11—Yesu anadyetsa khamu la anthu mozizwitsa (“amuna pafupifupi 5,000 anakhaladi pansi” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 6:10, nwtsty)
Yoh. 6:14, 24—Anthuwo anadziwa kuti Yesu ndi Mesiya ndipo tsiku lotsatira anayamba kumufunafuna (“mneneri” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 6:14, nwtsty)
Yoh. 6:25-27, 54, 60, 66-69—Popeza anthuwo ankatsatira Yesu komanso ophunzira ake ndi zolinga zolakwika, anakhumudwa ndi mawu amene iye analankhula (“chakudya chimene chimawonongeka . . . chopereka moyo wosatha” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 6:27, nwtsty; “wakudya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 6:54, nwtsty; w05 9/1 21 ¶13-14)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Yoh. 6:44—Kodi Atate amakokera bwanji anthu kwa iye? (“kukokedwa” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 6:44, nwtsty)
Yoh. 6:64—Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti ankadziwa “kuchokera pa chiyambi” kuti Yudasi adzamupereka? (“Yesu anadziwa . . . amene adzamupereka” “kuchokera pa chiyambi” mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 6:64, nwtsty)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yoh. 6:41-59
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri.
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. Sonyezani zimene mungachite ngati amene mukumulalikira wanena kuti ndi Mkhristu.
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Zinayenda Bwanji?: (5 min.) Nkhani yokambirana. Pemphani abale ndi alongo kuti afotokoze zosangalatsa zimene zinawachitikira pamene ankayesa kucheza ndi anthu kuti awalalikire.
“Sipanawonongeke Chilichonse”: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani mbali ina ya vidiyo yakuti, Nyumba Zabwino Kwambiri Zimene Zimalemekeza Yehova.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 5
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 95 ndi Pemphero