MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Sipanawonongeke Chilichonse
Yesu atadyetsa mozizwitsa amuna oposa 5,000 kuphatikizapo akazi ndi ana, anauza ophunzira ake kuti: “Sonkhanitsani zotsala zonse, kuti pasawonongeke chilichonse.” (Yoh. 6:12) Yesu anasonyeza kuyamikira zimene Yehova anam’patsa, popewa kuwononga zinthu.
Masiku anonso, Bungwe Lolamulira limayesetsa kutsanzira Yesu pogwiritsa ntchito mosamala zinthu zimene abale ndi alongo amapereka. Mwachitsanzo, pomanga likulu lathu la padziko lonse, m’tawuni ya Warwick ku New York, abale anasankha pulani yabwino n’cholinga choti pasamadzaonongeke ndalama zambiri.
KODI TINGAPEWE BWANJI KUWONONGA ZINTHU . . .
-
tikakhala pamisonkhano yachikhristu?
-
tikamatenga mabuku oti tizigwiritsa ntchito ifeyo? (km 5/09 3 ¶4)
-
tikamatenga mabuku oti tizigwiritsa ntchito tikamalalikira? (mwb17.02 “Tizigwiritsa Ntchito Mwanzeru Mabuku Ndiponso Magazini” ¶1)
-
tikakhala mu utumiki? (mwb17.02 4 ¶2, ndi bokosi)