Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzitsanzira Khristu pa Nkhani Yokhala Odzichepetsa Komanso Kuzindikira Malire Anu

Muzitsanzira Khristu pa Nkhani Yokhala Odzichepetsa Komanso Kuzindikira Malire Anu

Ngakhale kuti Yesu anali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako, anali wodzichepetsa ndipo ankazindikira malire ake popewa kulandira ulemu woyenera kupita kwa Yehova. (Yoh. 7:16-18) Koma mosiyana ndi Yesu, Satana sanali wodzichepetsa ndipo anakhala Mdyerekezi, dzina limene limatanthauza “wonenera ena zoipa.” (Yoh. 8:44) Afarisi anali ndi mtima wofanana ndi wa Satana chifukwa anali onyada ndipo ankanyoza aliyense amene ankakhulupirira Mesiya. (Yoh. 7:45-49) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu tikapatsidwa udindo kapena utumiki winawake mumpingo?

ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIKONDANA’​MUZIPEWA KUCHITA NSANJE KOMANSO KUDZITAMA, MBALI YOYAMBA, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

  • Kodi Alex anasonyeza bwanji mtima wonyada?

ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIKONDANA’​—MUZIPEWA KUCHITA NSANJE KOMANSO KUDZITAMA, MBALI YACHIWIRI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Alex anasonyeza bwanji kudzichepetsa?

    Kodi Alex analimbikitsa bwanji Bill ndi Carl?

ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIKONDANA’​—MUZIPEWA KUNYADA KOMANSO KUCHITA ZINTHU ZOSAYENERA, MBALI YOYAMBA, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

  • Kodi M’bale Harris anasonyeza bwanji kuti sankazindikira malire ake?

ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIKONDANA’​—MUZIPEWA KUNYADA KOMANSO KUCHITA ZINTHU ZOSAYENERA, MBALI YACHIWIRI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi M’bale Harris anasonyeza bwanji kuti amazindikira malire ake?

    Kodi chitsanzo chabwino cha M’bale Harris chinathandiza bwanji Faye?