Yesu Ankalemekeza Atate Wake
Yesu ankalemekeza Atate wake m’zochita komanso m’zolankhula zake. Iye ankafuna kuti anthu azidziwa kuti uthenga umene ankalalikira ndi wochokera kwa Mulungu. Choncho ankaphunzitsa zinthu zochokera m’Malemba ndipo nthawi zambiri ankakonda kugwira Malemba. Anthu akamamutamanda, iye ankakana ndipo ankawauza kuti atamande Yehova. Cholinga chake chachikulu chinali kukwaniritsa ntchito imene Yehova anamupatsa.—Yoh. 17:4.
Kodi tingatsanzire bwanji Yesu . . .
-
tikamaphunzitsa ena Baibulo komanso tikamakamba nkhani kumisonkhano?
-
ena akamatitamanda?
-
tikamaganizira mmene tingagwiritsire ntchito nthawi yathu?