KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI
Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri mu Utumiki
Yehova watipatsa ‘gulu lonse’ la abale ndi alongo athu kuti azitithandiza. (1Pe 5:9) Iwo angatithandize kuthana ndi mavuto omwe timakumana nawo mu utumiki. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anathandizidwa ndi Akula ndi Purisikila, Sila, Timoteyo ndi enanso.—Mac 18:1-5.
Kodi atumiki anzanu angakuthandizeni bwanji mu utumiki? Angakuthandizeni kudziwa zomwe mungayankhe munthu wina akanena zinthu zosonyeza kuti sakufuna kuti mukambirane naye, mmene mungachitire maulendo obwereza, kapenanso mmene mungayambitsire komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Ngati mukuona kuti mukufunika thandizo, ganizirani za munthu wina mumpingo wanu amene angakuthandizeni, ndipo m’pempheni. N’zosakayikitsa kuti nonse mudzapindula komanso mudzasangalala kwambiri.—Afi 1:25.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIGWIRITSA NTCHITO ZOMWE YEHOVA WATIPATSA KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA—ABALE ATHU, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi Anita anayesa kuchita chiyani pofuna kulimbikitsa Jane kuti akapezeke pamsonkhano wa mpingo?
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kupempha ofalitsa anzathu kuti tikhale limodzi tikamachititsa phunziro la Baibulo?
-
Kodi Jane ndi Mayi Mwira ankakonda zinthu zofanana ziti?
-
Kodi atumiki anzanu angakuthandizeni kukhala ndi maluso otani mu utumiki?