Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKRISTU

Muzikumbukira Yehova Nthawi Zonse

Muzikumbukira Yehova Nthawi Zonse

Ngati ntchito ikusowa, zikhoza kukhala zovuta kuika zinthu zokhudza Ufumu komanso chilungamo cha Mulungu pa malo oyamba m’moyo mwathu. Tikhoza kuyesedwa kuti tivomere ntchito imene ingatichititse kuti tisamakhale ndi nthawi yokwanira yotumikira Yehova kapenanso yosemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Komabe tizikhulupirira kuti Yehova amasonyeza mphamvu zake “kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2Mb 16:9) Palibe chilichonse chimene chingalepheretse Atate wathu wachikondi kutithandiza komanso kutipatsa zonse zomwe timafunikira. (Aro 8:32) Choncho tikamaganizira za mtundu wa ntchito imene tikufuna kugwira, tizidalira kwambiri Yehova ndipo cholinga chathu chizikhala kupitirizabe kumutumikira.​—Sl 16:8.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIGWIRA NTCHITO NDI MOYO WONSE NGATI KUTI MUKUGWIRIRA YEHOVA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani Jason anakana kulandira chiphuphu?

  • Kodi tingagwiritse ntchito bwanji lemba la Akolose 3:23?

  • Kodi chitsanzo chabwino cha Jason chinathandiza bwanji Thomas?

  • Muzilola kuti Yehova azikuthandizani mukamasankha zochita

    Kodi tingagwiritse ntchito bwanji lemba la Mateyu 6:22?