Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzilalikira Uthenga Wabwino Wakuti Dziko Labwino Layandikira

Muzilalikira Uthenga Wabwino Wakuti Dziko Labwino Layandikira

M’mwezi wa November tidzagwira ntchito yapadera yolalikira uthenga wabwino wakuti dziko labwino layandikira. (Sl 37:10, 11; Chv 21:3-5) Mukhoza kusintha zina ndi zina pa moyo wanu kuti mudzakhale ndi nthawi yokwanira yogwira nawo ntchitoyi. Ngati mudzafunsire upainiya wothandiza m’mwezi umenewu, mukhoza kudzasankha wa maola 30 kapena 50.

Konzekerani lemba lomwe limafotokoza za dziko latsopano loti mudzakambirane ndi anthu ambiri. Mukamasankha vesi m’Baibulo, muziganizira zimene anthu a m’dera lanu angachite nazo chidwi. Ngati munthu wasonyeza chidwi pa ulendo woyamba, m’patseni Nsanja ya Olonda Na. 2 2021. Ndiyeno pasanapite nthawi, mudzakambiranenso ndi munthuyo n’cholinga choti mudzayambe kuphunzira naye Baibulo pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kugwira nawo ntchito yolengeza “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.”​—Yes 52:7.

ONERANI VIDIYO YA NYIMBO YAKUTI DZIKO LATSOPANO LOMWE LIKUBWERA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi kamtsikanaka kakuganizira zinthu zabwino ziti zam’tsogolo?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene inuyo mukuyembekezera m’dziko latsopano?

  • Kodi kuganizira mozama zimene mukuyembekezera m’tsogolomu kungakuthandizeni bwanji kukonzekera ntchito yapadera yomwe tidzakhale nayo mu November?​—Lu 6:45