Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Muziteteza Cholowa Chanu Chomwe Ndi Chamtengo Wapatali

Muziteteza Cholowa Chanu Chomwe Ndi Chamtengo Wapatali

Kalebe anateteza cholowa chake pothamangitsa adani ake omwe anali amphamvu (Yos 15:14; it-1 1083 ¶3)

Aisiraeli ena sanateteze cholowa chawo kwa anthu omwe sankalambira Yehova (Yos 16:10; it-1 848)

Yehova anathandiza anthu omwe ankafunitsitsa kuteteza cholowa chawo (De 20:1-4; Yos 17:17, 18; it-1 402 ¶3)

Yehova anapereka kwa Akhristu onse cholowa chamtengo wapatali, chomwe ndi moyo wosatha. Kuti titeteze cholowachi tiziyesetsa kukana mayesero, ndipo zimenezi zingatheke tikamaphunzira Baibulo patokha, tikamapezeka pamisonkhano, tikamalalikira komanso tikamapemphera.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndikuteteza cholowa changa?’