Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Pitirizani Kuphunzitsa Mphamvu Zanu za Kuzindikira

Pitirizani Kuphunzitsa Mphamvu Zanu za Kuzindikira

Munthu amene amachita masewera othamanga amafunika kumadziphunzitsa kuti akhalebe ndi luso. Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kumachita khama kuti tipitirize kuphunzitsa mphamvu zathu za kuzindikira. (Ahe 5:14) Ngakhale kuti nthawi zina tikhoza kukhala ndi maganizo ofuna kutengera zimene ena asankha, tiyenera kumadziphunzitsa kuti tiziganiza komanso kusankha zochita patokha. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.​—Aro 14:12.

Sitikuyenera kuganiza kuti tikhoza kupanga zosankha zabwino chabe chifukwa chakuti tinabatizidwa kalekale. Kuti tizisankha zinthu mwanzeru, tiyenera kumadalira Yehova, Mawu ake, komanso gulu lake.​—Yos 1:7, 8; Miy 3:5, 6; Mt 24:45.

ONERANI VIDIYO YAKUTI “KHALANI NDI CHIKUMBUMTIMA CHABWINO,” NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Emma ankafunika kusankha chiyani?

  • N’chifukwa chiyani sitiyenera kusankhira ena zochita pazinthu zomwe aliyense akufunika kusankha yekha potengera chikumbumtima chake?

  • Kodi ndi malangizo anzeru ati amene banja lina linapereka kwa Emma?

  • Kodi Emma anapeza kuti malangizo othandiza okhudza vuto lomwe anakumana nalo?