Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muzigwiritsa Ntchito Zinthu Zofufuzira

Muzigwiritsa Ntchito Zinthu Zofufuzira

Yehova watipatsa zinthu zomwe zimatithandiza kuphunzitsa mwaluso monga mavidiyo, timapepala, magazini, timabuku, mabuku komanso Baibulo. (2Ti 3:16) Watipatsanso zinthu zofufuzira zomwe zimatithandiza kufotokoza Malemba momveka bwino. Zinthu zake ndi monga Watchtower Library, JW Library®, LAIBULALE YA PA INTANETI ndi Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani.

Mukamafufuza mfundo za m’Baibulo pogwiritsa ntchito zinthu zofufuzira zomwe tili nazo, mudzakhala osangalala kwambiri. Muziyesetsa kuphunzitsa ophunzira anu kudziwa mmene angagwiritsire ntchito zinthuzi, ndipo nawonso adzakhala osangalala akamapeza mayankho a m’Baibulo pawokha.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIGWIRITSA NTCHITO ZOMWE YEHOVA WATIPATSA KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA​MUZIGWIRITSA NTCHITO ZINTHU ZOFUFUZIRA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Jane anatsutsa chiyani zokhudza chilengedwe?

  • Kodi Anita anapeza kuti mfundo zokhudza nkhaniyo?

  • Kufufuza komanso kuuza ena mfundo za m’Baibulo kumatithandiza kukhala osangalala

    Kodi Anita anasankha bwanji mfundo zomwe zinali zothandiza kwa Jane?

  • Kodi kugwiritsa ntchito zinthu zofufuzira kunathandiza bwanji Anita?