September 27–October 3
YOSWA 6-7
Nyimbo Na. 144 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Musamaone Zinthu Zopanda Pake”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Yos 6:20—Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti mzinda wakale wa Yeriko unagonjetsedwa m’kanthawi kochepa? (w15 11/15 13 ¶2-3)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) Yos 6:1-14 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 12)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza. Yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? (th phunziro 9)
Phunziro la Baibulo: (5 min.) lffi phunziro 01 mfundo 3 (th phunziro 8)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zimene Gulu Lathu Lachita: (5 min.) Onerani vidiyo ya Zimene Gulu Lathu Lachita ya September.
Kusamvera Mwadala N’koopsa: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani mbali ina ya vidiyo yakuti ‘Palibe Ngakhale Mawu Amodzi Omwe Sanakwaniritsidwe.’ Ndipo kenako funsani mafunso otsatirawa: Kodi Yehova anapereka lamulo lomveka bwino liti lokhudza mzinda wa Yeriko? Kodi Akani ndi anthu a m’banja lake anachita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani? Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi? Limbikitsani onse kuti akaonere vidiyo yonse kunyumba kwawo.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lvs mutu 5 ndime 11-15, mawu akumapeto 18
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 36 ndi Pemphero