September 6-12
DEUTERONOMO 33-34
Nyimbo Na. 150 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Muzithawira ‘M’manja a Yehova Amene Adzakhalapo Mpaka Kalekale’”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
De 34:6—N’chifukwa chiyani Yehova sanauze anthu malo enieni amene Mose anaikidwa? (it-2 439 ¶3)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) De 33:1-17 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Ulendo Woyamba: Baibulo—2Ti 3:16, 17. Muziimitsa vidiyoyi nthawi iliyonse imene pali chizindikiro chosonyeza kuti muime n’kufunsa omvera mafunso omwe ali muvidiyoyi.
Ulendo Woyamba: (3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. (th phunziro 1)
Ulendo Woyamba: (5 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako mugawireni kabuku kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, ndipo yambitsani phunziro la Baibulo. (th phunziro 3)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzigwiritsa Ntchito Kabuku Ndi Buku Lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale mu Utumiki”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Sangalalani Pophunzira Baibulo. Ngati nthawi ilipo, tchulani zinthu zina zimene zikupezeka m’buku latsopanoli. Limbikitsani onse kuti aphunzire mitu yonse ya m’bukuli paokha kapena pa Kulambira kwa Pabanja.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lvs mutu 4 ndime 12-17, mawu akumapeto 13-15
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 48 ndi Pemphero