Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Banja Ndi Mgwirizano wa Moyo Wonse

Banja Ndi Mgwirizano wa Moyo Wonse

Mabanja a Chikhristu amene amayenda bwino amalemekeza Mulungu, ndiponso onse mwamuna ndi mkazi, amakhala osangalala. (Mko 10:9) Kuti Mkhristu adzakhale ndi banja lolimba komanso losangalala, ayenera kutsatira mfundo za m’Baibulo akamasankha munthu wokwatirana naye.

Musakhale pachibwenzi ndi wina aliyense mpaka ‘mutapitirira pachimake pa unyamata,’ yomwe ndi nthawi imene chilakolako cha kugonana chimakhala champhamvu kwambiri ndipo chingakupangitseni kuti musamaganize bwino. (1Ak 7:36) Muzigwiritsa ntchito mwanzeru nthawi imene simunalowe m’banja polimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova komanso kukulitsa makhalidwe amene Akhristu ayenera kukhala nawo. Zimenezi zidzakuthandizani kuti mudzakhale ndi banja losangalala.

Musanatsimikize zokwatirana ndi winawake, muzikhala ndi nthawi yokwanira kuti mudziwe bwino “munthu wobisika wamumtima.” (1Pe 3:4) Ngati mwayamba kukayikira kwambiri kuti munthu amene mukufuna kukwatirana naye alidi woyenerera, kambiranani naye. Mofanana ndi mmene zimakhalira ndi mabwenzi apamtima, anthu okwatirana ayenera kumaganizira kwambiri zimene iwowo angachitire mnzawoyo, osati zimene angawachitire. (Afi 2:3, 4) Ngati mutamatsatira mfundo za m’Baibulo musanalowe m’banja, zidzakhala zosavuta kuti mukadzakwatira mudzapitirize, ndipo zimenezi zidzakuthandizani kuti mudzakhale ndi banja losangalala.

ONERANI VIDIYO YAKUTI KUKONZEKERA KULOWA M’BANJA​—GAWO 3: “KUWERENGERA NDALAMA ZIMENE MUDZAWONONGE,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi chibwenzi cha mlongoyu ndi Shane chinkayenda bwanji?

  • Kodi mlongoyu anazindikira chiyani pamene ankayamba kumudziwa bwino?

  • Kodi makolo ake anamuthandiza bwanji, nanga anasankha bwanji zinthu mwanzeru?