MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kufikira Pamene Adzakhalenso Ndi Moyo
Munthu amene timam’konda akamwalira timatonthozedwa tikaganizira kuti adzaukitsidwa. Ngakhale zili choncho, uchimo komanso imfa zili ngati chophimba chimene chimatiphimba tonsefe ndipo chimatisowetsa mtendere. (Yes 25:7, 8) N’chifukwa chake “chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa.” (Aro 8:22) Kodi tingatani kuti tipirire imfa ya okondedwa athu kufikira pamene adzakhalenso ndi moyo? M’Mawu a Mulungu muli mfundo zimene zingatithandize.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE MUNGACHITE MUKAFEREDWA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi Danielle komanso Masahiro ndi Yoshimi anakumana ndi mavuto otani?
-
Kodi mfundo 5 zotchulidwa mu vidiyoyi zinawathandiza bwanji?
-
Kodi ndi ndani amene amatitonthoza?—2Ak 1:3, 4