MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzidalira Yehova Mukakumana ndi Mavuto Azachuma
Moyo m’masiku otsirizawa wangodzaza ndi mavuto. Pamene tikuyandikira mapeto a dzikoli, mavuto aziwonjezereka kwambiri ndipo nthawi zina tikhoza kumasowa zinthu zofunika pa moyo. (Hab 3:16-18) Kodi n’chiyani chingatithandize kupirira tikakumana ndi mavuto azachuma? Tiyenera kupitiriza kudalira Yehova Mulungu wathu. Iye analonjeza kuti adzasamalira atumiki ake ndipo adzawapatsa zonse zimene amafunikira zivute zitani.—Sl 37:18, 19; Ahe 13:5, 6.
Zimene mungachite:
-
Muzipempha Yehova kuti akutsogolereni, akupatseni nzeru komanso akuthandizeni.—Sl 62:8
-
Muzikhala okonzeka kugwira ntchito iliyonse ngakhale imene simunagwirepo.—g 1/10 8-9, mabokosi
-
Muzichita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse, kuphatikizapo kuwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse, kupezeka pa misonkhano ya mpingo komanso kugwira nawo ntchito yolalikira
ONERANI VIDIYO YAKUTI MANGANI NYUMBA YOLIMBA—‘MUZIKHALA OKHUTIRA NDI ZIMENE MULI NAZO,’ KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi ndi mavuto ati amene mabanja ena anakumana nawo?
-
Kodi chinthu chofunika kwambiri pa moyo n’chiyani?
-
Kodi tingathandize bwanji anthu amene akukumana ndi mavuto azachuma?