CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Tizitamanda Yehova Chifukwa ndi Wanzeru
Yehova anapatsa Solomo nzeru zapadera (1Mf 10:1-3; w99 7/1 30 ¶6)
Mfumukazi ya ku Sheba inachita chidwi ndi nzeru zimene Yehova anapatsa Solomo (1Mf 10:4, 5; w99 11/1 20 ¶6)
Mfumukazi ya ku Sheba inatamanda Yehova chifukwa chosankha Solomo kuti akhale mfumu (1Mf 10:6-9; w99 7/1 30-31)
Mofanana ndi mfumukazi ya ku Sheba, nafenso tingasonyeze kuti timayamikira nzeru zimene Mulungu anatipatsa. Njira imodzi ndi kugwiritsa ntchito zimene Yesu anaphunzitsa komanso kuchita zonse zomwe tingathe kuti titengere chitsanzo chake. (Mt 12:42; 1Pe 2:21) Njira inanso ndi kuuza ena nzeru za Mulungu tikakhala mu utumiki.