Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Moyo Ukafika Povuta

Moyo Ukafika Povuta

Pamene ankakumana ndi mayesero, Yobu anayerekezera moyo ndi ntchito yokakamiza (Yob 7:1; w06 3/15 14 ¶10)

Mavuto amene Yobu ankakumana nawo anam’chititsa kufotokoza momasuka mmene ankamvera (Yob 7:11)

Anafika mpaka ponena kuti akufuna kufa (Yob 7:16; w20.12 16 ¶1)

Mukaona kuti moyo wanu wafika povuta kwambiri, muzipemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima, kumuuza zonse zomwe zili mumtima mwanu, komanso muzifotokozera mnzanu wodalirika mmene mukumvera. Imeneyi ikhoza kukhala njira yoyamba imene ingakuthandizeni kuti muyambenso kumva bwino.—g 1/12 16-17.